Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 14:41-54 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. napalitse nyumba m'kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mudzi dothi adapalako;

42. natenge miyala yina, naikhazike m'male mwa miyala ija; natenge dothi tina, namatenso nyumbayo.

43. Ndipo ikabweranso nthenda, nibukanso m'nyumba atagumula miyala, ndipo atapala m'nyumba namatanso;

44. pamenepo wansembe alowe naonemo, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'nyumba, ndiyo khate lonyeka m'nyumba; ndiyo yodetsedwa.

45. Ndipo apasule nyumbayo, miyala yace, ndi mitengo yace, ndi dothi lace lonse kumudzi kuzitaya ku malo akuda.

46. Ndiponso iye wakulowa m'nyumba masiku ace iriyotsekedwa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

47. Ndipo iye wakugona m'nyumbayo atsuke zobvala zace; ndi iye wakudya m'nyumbayo atsuke zobvala zace.

48. Ndipo wansembe akalowa, nakaona, ndipo taonani, nthenda siinakula m'nyumba, ataimata nyumba; wansembe aiche nyumbayo yoyera, popeza nthenda yaleka.

49. Pamenepo atenge mbalame ziwiri, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, kuti ayeretse nazo nyumbayo;

50. naphe mbalame imodzi m'mbale yadothi, pamwamba pa madzi oyenda;

51. natenge mtengo wamkungudza ndi hisope, ndi ubweya wofiira, ndi mbalame yamoyo, nazibviike m'mwazi wa mbalame yakuphayo, ndi m'madzi oyenda, nawaze kasanu ndi kawiri m'nyumba;

52. nayeretsenyumbandi mwazi wa mbalame, ndi madzi oyenda, ndi mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira.

53. Koma ataye mbalame yamoyo kunja kwa mudzi kuthengo koyera; motero aicitire coitetezera nyumbayo; ndipo idzakhala yoyera.

54. Ici ndi cilamulo ca nthenda iri yonse yakhate, ndi yamfundu;

Werengani mutu wathunthu Levitiko 14