Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 14:41-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. napalitse nyumba m'kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mudzi dothi adapalako;

42. natenge miyala yina, naikhazike m'male mwa miyala ija; natenge dothi tina, namatenso nyumbayo.

43. Ndipo ikabweranso nthenda, nibukanso m'nyumba atagumula miyala, ndipo atapala m'nyumba namatanso;

44. pamenepo wansembe alowe naonemo, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'nyumba, ndiyo khate lonyeka m'nyumba; ndiyo yodetsedwa.

45. Ndipo apasule nyumbayo, miyala yace, ndi mitengo yace, ndi dothi lace lonse kumudzi kuzitaya ku malo akuda.

46. Ndiponso iye wakulowa m'nyumba masiku ace iriyotsekedwa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

47. Ndipo iye wakugona m'nyumbayo atsuke zobvala zace; ndi iye wakudya m'nyumbayo atsuke zobvala zace.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 14