Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 14:36-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ndipo wansembe aziuza kuti aturutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse ziri m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;

37. naone nthendayo, ndipo taonani, nthenda ikakhala yosumbudzuka m'makoma a nyumba yobiriwira kapena yofiira, ndipo maonekedwe ace yakumba kubzola khoma;

38. pamenepo wansembe azituruka ku khomo la nyumba, natseke nyumbayo masiku asanu ndi awiri;

39. ndipo wansembe abwerenso tsiku lacisanu ndi ciwiri, naonenso, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'makoma a nyumba;

40. pamenepo wansembe auze kuti agumule miyalayi pali nthenda, naitayire ku malo akuda kunja kwa mudzi;

41. napalitse nyumba m'kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mudzi dothi adapalako;

42. natenge miyala yina, naikhazike m'male mwa miyala ija; natenge dothi tina, namatenso nyumbayo.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 14