33. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
34. Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanu lanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanu lanu;
35. pamenepo mwini nyumbayo adzauze wansembe, kuti, Ndiyesa muli ngati nthenda m'nyumba.
36. Ndipo wansembe aziuza kuti aturutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse ziri m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;
37. naone nthendayo, ndipo taonani, nthenda ikakhala yosumbudzuka m'makoma a nyumba yobiriwira kapena yofiira, ndipo maonekedwe ace yakumba kubzola khoma;