Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 14:22-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yaucimo, ndi linzace la nsembe yopsereza.

23. Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu abwere nao kwa wansembe, ku khomo la cihema cokomanako, pamaso pa Yehova.

24. Ndipo wansembe atenge mwana wa nkhosa wa nsembe yoparamula, ndi muyeso wa mafuta, ndipo wansembe aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova;

25. naphe mwana wa nkhosa wa nsembe yoparamula, ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yoparamula, naupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye akuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja;

26. ndipo wansembe athireko mafuta aja m'cikhato cace camanzere ca iye mwini;

27. ndipo wansembe awazeko mafuta aja ali m'dzanja lace lamanzere ndi cala cace ca dzanja lamanja, kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova;

28. ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lace pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca: dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa usembe yoparamula;

29. ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumcitira comtetezera pamaso pa Yehova.

30. Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo, limodzi la nsembe yaucimo, ndi tina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa;

31. ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova.

32. Ici ndi cilamulo ca iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pace.

33. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

34. Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanu lanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanu lanu;

35. pamenepo mwini nyumbayo adzauze wansembe, kuti, Ndiyesa muli ngati nthenda m'nyumba.

36. Ndipo wansembe aziuza kuti aturutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse ziri m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;

37. naone nthendayo, ndipo taonani, nthenda ikakhala yosumbudzuka m'makoma a nyumba yobiriwira kapena yofiira, ndipo maonekedwe ace yakumba kubzola khoma;

38. pamenepo wansembe azituruka ku khomo la nyumba, natseke nyumbayo masiku asanu ndi awiri;

39. ndipo wansembe abwerenso tsiku lacisanu ndi ciwiri, naonenso, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'makoma a nyumba;

40. pamenepo wansembe auze kuti agumule miyalayi pali nthenda, naitayire ku malo akuda kunja kwa mudzi;

41. napalitse nyumba m'kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mudzi dothi adapalako;

Werengani mutu wathunthu Levitiko 14