Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 14:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati,

2. Cilamulo ca wakhate tsiku la kumyeretsa kwace ndi ici: azidza naye kwa wansembe;

3. ndipo wansembe aturuke kumka kunja kwa cigono; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nthenda Yakhate yapola pa wakhateyo;

4. pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi, ubweya wofiira, ndi hisope;

5. ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m'mbale yadothi pamwamba pa madzi oyenda;

6. natenge nbalame yamoyo, ndi mtengo wankungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, nazibviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda;

Werengani mutu wathunthu Levitiko 14