Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 11:5-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndi mbira, ingakhale ibzikula koma yosagawanika ciboda, muiyese yodetsedwa.

6. Ndi kalulu, popeza abzikula koma wosagawanika ciboda, mumuyese wodetsedwa.

7. Ndi nkhumba, popeza igawanika ciboda, nikhala yogawanikadi ciboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa.

8. Nyama yace musamaidya, mitembo yace musamaikhudza; muziyese zodetsedwa.

9. Mwa zonse ziri m'madzi muyenera kumadya izi: ziri zonse ziti nazo zipsepse ndi mamba m'madzi, m'nyanja, ndi m'mitsinje, zimenezo muyenera kumadya.

10. Koma ziti zonse ziribe zipsepse ndi mamba m'nyanja, ndi m'mitsinje, mwa zonse zokwawa za m'madzi, ndi mwa zamoyo zonse ziri m'madzi, muziziyesa zonyansa;

11. inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.

12. Ziri zonse zopanda zipsepse kapena mamba m'madzimo muziyese zonyansa.

13. Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; siziyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi cikambi;

14. ndi muimba, ndi mphamba mwa mtundu wace;

15. kungubwi mwa mtundu wace;

16. ndi nthiwatiwa, ndi cipudo, ndi kakoa, ndi kabawi mwa mtundu wace;

17. ndi nkhutunkhutu ndi nswankhono ndi mancici;

18. tsekwe, bvuwo, ndi dembu;

19. indwa, ndi cimeza monga mwa mtundu wace, ndi sadzu, ndi mleme.

20. Zokwawa zonse zakuuluka zokhala ndi miyendo inai, muziyesa izi zonyansa,

Werengani mutu wathunthu Levitiko 11