Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 11:13-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; siziyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi cikambi;

14. ndi muimba, ndi mphamba mwa mtundu wace;

15. kungubwi mwa mtundu wace;

16. ndi nthiwatiwa, ndi cipudo, ndi kakoa, ndi kabawi mwa mtundu wace;

17. ndi nkhutunkhutu ndi nswankhono ndi mancici;

18. tsekwe, bvuwo, ndi dembu;

19. indwa, ndi cimeza monga mwa mtundu wace, ndi sadzu, ndi mleme.

20. Zokwawa zonse zakuuluka zokhala ndi miyendo inai, muziyesa izi zonyansa,

21. Koma muyenera kudya izi mwa zokwawa zonse zakuuluka, zokhala ndi miyendo inai, zokhala ndi miyendo pa mapazi ao, ya kuthumpha nayo pansi; mwa zimenezi muyenera kudya izi:

22. dzombe mwa mtundu wace, ndi cirimamine mwa mitundu yace, ndi njenjete mwa mtundu wace ndi tsokonombwe mwa mitundu yace.

23. Koma zokwawa zonse zakuuluka, za miyendo inai, muziyese zonyansa.

24. Ndipo izi zikudetsani: ali yense akhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo;

25. ndipo ali yense akanyamulako nyama ya mtembo wace azitsuka zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

26. Nyama iri yonse yakugawanika ciboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; ali yense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa.

27. Ndipo iri yonse iyenda yopanda ciboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; ali yense wokhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 11