Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 11:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati nao,

2. Nenani ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse ziri pa dziko lapansi.

3. Nyama iri yonse yogawanika ciboda, nikhala yogawanikadi ciboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya.

4. Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika ciboda; ngamila, angakhale abzikula, koma yosagawanika ciboda, muziiyesa yodetsedwa.

5. Ndi mbira, ingakhale ibzikula koma yosagawanika ciboda, muiyese yodetsedwa.

6. Ndi kalulu, popeza abzikula koma wosagawanika ciboda, mumuyese wodetsedwa.

7. Ndi nkhumba, popeza igawanika ciboda, nikhala yogawanikadi ciboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa.

8. Nyama yace musamaidya, mitembo yace musamaikhudza; muziyese zodetsedwa.

9. Mwa zonse ziri m'madzi muyenera kumadya izi: ziri zonse ziti nazo zipsepse ndi mamba m'madzi, m'nyanja, ndi m'mitsinje, zimenezo muyenera kumadya.

10. Koma ziti zonse ziribe zipsepse ndi mamba m'nyanja, ndi m'mitsinje, mwa zonse zokwawa za m'madzi, ndi mwa zamoyo zonse ziri m'madzi, muziziyesa zonyansa;

11. inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 11