7. Ndiye Mkanani, m'dzanja lace muli miyeso yonyenga, akonda kusautsa.
8. Ndipo Efraimu anati, Zedi ndasanduka wolemera, ndadzionera cuma m'nchito zonse ndinazigwira; sadzapeza mwa ine mphulupulu yokhala cimo.
9. Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako cicokere dziko la Aigupto, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a masonkhano oikika.
10. Ndalankhulanso ndi aneneri, ndipo Ine ndacurukitsa masomphenya; ndi pa dzanja la aneneri ndinanena ndi mafanizo.
11. Kodi Gileadi ndiye wopanda pace? akhala acabe konse; m'Giligala aphera nsembe yang'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'micera ya munda.
12. Ndipo Yakobo anathawira ku thengo la Aramu, ndi Israyeli anagwira nchito cifukwa ca mkazi, ndi cifukwa ca mkazi anaweta nkhosa.