9. Sindidzacita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efraimu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi.
10. Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kucokera kumadzulo.
11. Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Aigupto, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asuri; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova.
12. Efraimu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israyeli ndi cinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.