Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 11:4-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za cikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira cakudya.

5. Iye sadzabwerera kumka ku dziko la Aigupto, koma Asuri adzakhala mfumu yace, popeza anakana kubwera.

6. Ndi lupanga lidzagwera midzi yace, lidzatha mipiringidzo yace, ndi kuononga cifukwa ca uphungu wao.

7. Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; cinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense.

8. Ndidzakusiya bwanji, Efraimu? ndidzakupereka bwanji, Israyeli? ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zacifundo zanga zilira zonse pamodzi.

9. Sindidzacita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efraimu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi.

10. Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kucokera kumadzulo.

11. Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Aigupto, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asuri; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova.

12. Efraimu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israyeli ndi cinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 11