Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 10:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Israyeli ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinacurukira zipatso zace, momwemo anacurukitsa maguwa a nsembe ace; monga mwa kukoma kwace kwa dziko lace anapanga zoimiritsa zokoma.

2. Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka oparamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.

3. Pakuti tsopano adzati, Tiribe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzaticitira ciani?

4. Anena mau akulumbira monama, pakucita mapangano momwemo; ciweruzo ciphuka ngati zitsamba zowawa m'micera ya munda.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 10