Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hagai 2:6-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe;

7. ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.

8. Siliva ndi wanga, golidi ndi wanga, ati Yehova wa makamu.

9. Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.

10. Tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi wacisanu ndi cinai, caka caciwiri ca Dariyo, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,

11. Atero Yehova wa makamu: Funsatu ansembe za cilamulo, ndi kuti,

12. Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena cakudya ciri conse, ndi ngudulira, kodi cisandulika copatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.

13. Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa.

14. Ndipo Hagai anayankha, nati, Momwemo anthu awa, ndi momwemo mtundu uwu pamaso panga, ati Yehova; ndi momwemo nchito iri yonse ya manja ao; ndi ici acipereka, ciri codetsedwa.

15. Ndipo tsono, samalirani, kuyambira lero ndi m'tsogolomo, kuti, kusanaikidwe mwala pa mwala m'Kacisi wa Yehova,

16. pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku coponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha.

17. Ndinakukanthani ndi cinsikwi ndi cinoni ndi matalala m'nchito zonse za manja anu, koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

18. Musamalire, kuyambira lero ndi m'tsogolo, kuyambira tsiku la makumi awiri ndi cinai la mwezi wacisanu ndi cinai, kuyambira tsiku lija anamanga maziko a Kacisi wa Yehova, samalirani.

19. Kodi mbeu ikali m'nkhokwe? Ngakhale mpesa, ndi mkuyu, ndi khangaza ndi mzitona sizinabala; kuyambira lero lino ndidzakudalitsani.

20. Ndipo mau a Yehova anadza nthawi yaciwiri kwa Hagai tsiku la makumi awiri la mwezi, ndi kuti,

21. Nena ndi Zerubabele ciwanga ca Yuda, kuti, Ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi;

Werengani mutu wathunthu Hagai 2