Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hagai 2:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo tsono, samalirani, kuyambira lero ndi m'tsogolomo, kuti, kusanaikidwe mwala pa mwala m'Kacisi wa Yehova,

16. pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku coponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha.

17. Ndinakukanthani ndi cinsikwi ndi cinoni ndi matalala m'nchito zonse za manja anu, koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

18. Musamalire, kuyambira lero ndi m'tsogolo, kuyambira tsiku la makumi awiri ndi cinai la mwezi wacisanu ndi cinai, kuyambira tsiku lija anamanga maziko a Kacisi wa Yehova, samalirani.

19. Kodi mbeu ikali m'nkhokwe? Ngakhale mpesa, ndi mkuyu, ndi khangaza ndi mzitona sizinabala; kuyambira lero lino ndidzakudalitsani.

20. Ndipo mau a Yehova anadza nthawi yaciwiri kwa Hagai tsiku la makumi awiri la mwezi, ndi kuti,

21. Nena ndi Zerubabele ciwanga ca Yuda, kuti, Ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi;

22. ndipo ndidzagubuduza mipando yacifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magareta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wace.

23. Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealitiyeli, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu.

Werengani mutu wathunthu Hagai 2