Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hagai 1:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Kwerani ku dziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.

9. Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang'ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Cifukwa ninji? ati Yehova wa makamu. Cifukwa ca nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwace.

10. M'mwemo cifukwa ca inu kumwamba kukaniza mame, ndi nthaka ikaniza zipatso zace.

11. Ndipo ndinaitana cirala cidzere dziko, ndi mapiri, ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zimene ibala nthaka, ndi anthu, ndi zoweta, ndi nchito zonse za manja.

12. Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe, ndi otsala onse a anthu, anamvera mau a Yehova Mulungu wao, ndi mau a Hagai mneneri, monga Yehova Mulungu wao adamtuma; ndipo anthu anaopa pamaso pa Yehova.

13. Ndipo Hagai mthenga wa Yehova m'uthenga wa Yehova ananena ndi anthu, ndi kuti, Ine ndiri nanu, ati Yehova.

14. Ndipo Yehova anautsa mzimu wa Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ciwanga ca Yuda, ndi mzimu wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi mzimu wa otsala onse a anthu, ndipo anadza nagwira nchito m'nyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wao,

15. tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi, mwezi wacisanu ndi cimodzi, caka caciwiri ca mfumu Dariyo.

Werengani mutu wathunthu Hagai 1