Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hagai 1:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Cifukwa cace tsono, atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.

6. Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudzibveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa nchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka.

7. Atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.

8. Kwerani ku dziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.

9. Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang'ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Cifukwa ninji? ati Yehova wa makamu. Cifukwa ca nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwace.

Werengani mutu wathunthu Hagai 1