Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hagai 1:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. CAKA caciwiri ca mfumu Dariyo, mwezi wacisanu ndi cimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ciwanga ca Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,

2. Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova.

3. Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,

4. Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhala m'nyumba zanu zocingidwa m'katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka?

5. Cifukwa cace tsono, atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.

6. Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudzibveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa nchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka.

7. Atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.

8. Kwerani ku dziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Hagai 1