Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Habakuku 1:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. KATUNDU adamuona Habakuku

2. Yehova, ndidzapfuula mpaka liti osamva Inu? ndipfuulira kwa Inu za ciwawa, koma simupulumutsa.

3. Mundionetseranji zopanda pace, ndi kundionetsa zobvuta? pakuti kufunkha ndi ciwawa ziri pamaso panga; ndipo pali ndeli nauka makani.

4. Pakuti cilamulo calekeka, ndi ciweruzo siciturukira konse; popeza woipa azinga wolungama, cifukwa cace ciweruzo cituruka copindika.

5. Penyani mwa amitundu, penyetsetsani, nimudabwe kwakukuru, pakuti ndicita nchito masiku anu, imene simudzabvomera cinkana akufotokozerani.

6. Pakuti taonani, ndiukitsa Akasidi, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira, pa citando ca dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwao mwao.

7. Ali oopsa, acititsa mantha, ciweruzo cao ndi ukulu wao zituruka kwa iwo eni.

8. Akavalo ao aposa anyalugwe liwiro lao, aposa mimbulu ya madzulo ukali wao, ndipo apakavalo ao atanda; inde apakavalo ao afumira kutali; auluka ngati ciombankhanga cofulumira kudya.

9. Adzera ciwawa onsewo; nkhope zao zikhazikika zolunjika m'tsogolo; asonkhanitsa andende ngati mcenga,

10. Inde anyoza mafumu, aseka akalonga; aseka linga liri lonse; popeza aunjika dothi, nalilanda.

11. Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, oadzalakwa ndi kuparamula, iye amene aiyesa mphamvu yace mulungu wace.

Werengani mutu wathunthu Habakuku 1