Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 7:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri,

21. Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda pa dziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi, ndi anthu onse:

22. zonse zimene m'mphuno zao munali mpweya wa maimu wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa.

23. Ndipo zinaonongedwa zamoyo zimene zonse zinali pa dziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa pa dzikolapansi: anatsala Nowayekha ndi amene anali pamodzi naye m'cingalawa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 7