Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 7:13-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Tsiku lomwelo analowa m'cingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wace wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ace pamodzi nao:

14. iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa pa dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundu mitundu.

15. Ndipo zinalowa kwa Nowa m'cingalawamo ziwiri ziwiri zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo.

16. Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye.

17. Ndipo cigumula cinali pa dziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anacuruka natukula cingalawa, ndipo cinakwera pamwamba pa dziko lapansi.

18. Ndipo madzi anapambana, nacuruka ndithu pa dziko lapansi, ndipo cingalawa cinayandama pamadzi.

19. Ndipo madzi anapambana ndithu pa dziko lapansi; anamizidwa mapiri atari onse amene anali pansi pa thambo lonse.

Werengani mutu wathunthu Genesis 7