Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 7:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a cigumula anali pa dziko lapansi.

11. Caka ca mazana asanu ndi limodzi ca moyo wa Nowa, mwezi waciwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi akuru anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.

12. Ndipo mvula inali pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku.

13. Tsiku lomwelo analowa m'cingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wace wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ace pamodzi nao:

14. iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa pa dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundu mitundu.

15. Ndipo zinalowa kwa Nowa m'cingalawamo ziwiri ziwiri zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo.

16. Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye.

Werengani mutu wathunthu Genesis 7