Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 7:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi a ku nyumba ako onse m'cingalawamo; cifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno.

2. Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yace; ndi nyama zosadyedwa ziwiri ziwiri yamphongo ndi yaikazi yace.

3. Ndiposo mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo pa dziko lonse lapansi.

4. Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzabvumbitsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga pa dziko lapansi,

5. Ndipo anacita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova.

6. Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu ndi limodzi, pamene cigumula ca madzi cinali pa dziko lapansi.

7. Ndipo analowa Nowa ndi ana ace ndi mkazi wace ndi akazi a ana ace m'cingalawamo, cifukwa ca madzi a cigumula.

8. Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi,

9. zinalowa ziwiri ziwiri kwa Nowa m'cingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.

10. Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a cigumula anali pa dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 7