Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 50:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yosefe anagwapa nkhope ya atate wace, namlirira iye nampsompsona iye.

2. Ndipo Yosefe anauza akapolo ace asing'anga kutiakonze atate wace: ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israyeli.

3. Ndipo anatha masiku ace makumi anai a iye; cifukwa comweco amatsiriza masiku akukonza thupi; ndipo Aaigupto anamlira iye masiki makumi asanu ndi awiri.

4. Atapita masiku akumlira iye Yosefe anati kwa mbumba ya Farao kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamase panu, nenanitu m'makutu a Parae kuti,

5. Atate wanga anandilumbi ritsa ine, kuti, Taona, ndirinkufa m'manda m'mene ndadzikonzeran ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundi loletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabwe ranso.

Werengani mutu wathunthu Genesis 50