4. Masiku ace Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana amuna ndi akazi.
5. Masiku ace onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.
6. Ndipo Seti anakhala ndi moyo zaka zana kudza zisanu, nabala Enosi;
7. ndipo Seti anakhala ndi moyo, atabala Enosi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza zisanu ndi ziwiri: ndipo anabala ana amuna ndi akazi:
8. masiku ace onse a Seti anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi ndi ziwiri; ndipo anamwalira.
9. Ndipo Enosi anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi anai, nabala Kenani;
10. ndipo anakhala ndi moyo Enosi, atabala Kenani, zaka mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi zisanu: ndipo anabala ana amuna ndi akazi.
11. Masiku ace onse a Enosi anali mazana asanu ndi anai kudza zisanu; ndipo anamwalira.
12. Ndipo Kenani anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, ndipo anabala Mahalalele:
13. ndipo Kenani anakhala ndi moyo, atabala Mahalalele zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi anai, ndipo anabala ana amuna ndi akazi;
14. masiku ace onse a Kenani anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi; ndipo anamwalira.
15. Ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Yaredi;
16. ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo, atabala Yaredi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu, nabala ana amuna ndi akazi: