Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 5:22-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. ndipo Enoke anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana amuna ndi akazi;

23. masiku ace onse a Enoke anali mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi ndi zisanu;

24. ndipo Enoke anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga.

25. Ndipo Metusela anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi zisanu ndi ziwiri, nabala Lameke;

26. ndipo Metusela anakhala ndi moyo, atabala Lameke, zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala ana amuna ndi akazi:

27. masiku ace onse a Metusela anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinai; ndipo anamwalira.

28. Ndipo Lameke anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala mwana wamwamuna;

29. namucha dzina lace Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pa nchito zathu zobvuta za manja athu, cifukwa ca nthaka imene anaitemberera Yehova;

30. ndipo Lameke anakhala ndi moyo atabala Nowa, zaka mazana asanu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu, nabala ana amuna ndi akazi:

31. masiku ace onse a Lameke anali zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamwa lira.

32. Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu; ndipo Nowa anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti.

Werengani mutu wathunthu Genesis 5