20. masiku ace onse a Yaledi anali zaka mazana asanu ndi anai kudza maitumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri: ndipo anamwalira.
21. Ndipo Enoke anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela:
22. ndipo Enoke anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana amuna ndi akazi;
23. masiku ace onse a Enoke anali mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi ndi zisanu;
24. ndipo Enoke anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga.
25. Ndipo Metusela anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi zisanu ndi ziwiri, nabala Lameke;
26. ndipo Metusela anakhala ndi moyo, atabala Lameke, zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala ana amuna ndi akazi:
27. masiku ace onse a Metusela anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinai; ndipo anamwalira.
28. Ndipo Lameke anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala mwana wamwamuna;
29. namucha dzina lace Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pa nchito zathu zobvuta za manja athu, cifukwa ca nthaka imene anaitemberera Yehova;