13. ndipo Kenani anakhala ndi moyo, atabala Mahalalele zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi anai, ndipo anabala ana amuna ndi akazi;
14. masiku ace onse a Kenani anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi; ndipo anamwalira.
15. Ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Yaredi;
16. ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo, atabala Yaredi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu, nabala ana amuna ndi akazi:
17. masiku ace onse a Mahalalele anali zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu; ndipo anamwalira.
18. Ndipo Yaredi anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri, nabala Enoke;
19. ndipo Yaredi anakhala ndi moyo, atabala Enoke, zaka mazana asanu ndi atatu, nabala ana amuna ndi akazi;
20. masiku ace onse a Yaledi anali zaka mazana asanu ndi anai kudza maitumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri: ndipo anamwalira.
21. Ndipo Enoke anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela:
22. ndipo Enoke anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana amuna ndi akazi;