14. Isakara ndiye buru wolimba,Alinkugona pakati pa makola;
15. Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino,Ndi dziko kuti linali lokondweretsa;Ndipo anaweramitsa phewa lace kuti anyamule,Nakhala kapolo wakugwira nchito ya msonkho,
16. Dani adzaweruza anthu ace,Monga limodzi la mafuko a Israyeli.
17. Dani adzakhala njoka m'khwalala,Songo panjira,Imene iluma zitende za kavalo,Kuti womkwera wace agwe cambuyo.
18. Ndadikira cipulumutso canu, Yehova.
19. Ndi Gadi, acifwamba adzampsinja iye;Koma iye adzapsinja pa citende cao.
20. Ndi Aseri, cakudya cace ndico mafuta,Ndipo adzapereka zolongosoka zacifumu.