Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 46:17-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndi ana amuna a Aseri: Yimna, ndi Yisiva, ndi Yisivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Maliki eli.

18. Amenewa ndi ana a Zilipa, amene Labani anampatsa Leya mwana wace wamkazi, amenewo anambalira Yakobo, anthu khumi ndi asanu ndi mmodzi.

19. Ana a Rakele mkazi wace wa Yakobo: Yosefe ndi Benjamini.

20. Kwa Yosefe kunabadwa m'dziko la Aigupto Manase ndi Efraimu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.

21. Ndi ana amuna a Benjamini: Bela ndi Bekeri, ndi Asibeli, ndi Gera, ndi Namani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi.

22. Amenewo ndi ana a Rakele, amene anabadwira Yakobo; anthu onse ndiwo khumi ndi anai.

23. Ndi ana amuna a Dani: Husimu.

24. Ndi ana amuna a Nafitali: Yazeeli, ndi Guni, ndi Yezera ndi Silemu.

25. Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wace wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi awiri.

26. Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo m'Aigupto, amene anaturuka m'cuuno mwace, pamodzi ndi akazi a ana amuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;

27. ndi ana amuna a Yosefe, amene anambadwira iye m'Aigupto ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa m'Aigupto anali makumi asanu ndi awiri.

Werengani mutu wathunthu Genesis 46