13. Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse m'Aigupto, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.
14. Ndipo anagwa pakhosi pace pa Benjamini, nalira; ndipo Benjamini nalira pakhosi pace.
15. Ndipo anampsompsona abale ace onse, nalilira iwo; ndipo pambuyo pace abale ace onse anaceza naye.
16. Ndipo mbiri yace inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ace a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ace.
17. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Citani ici; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani;
18. katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Aigupto, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.
19. Tsopano mwalamulidwa citani ici; muwatengere ana anu ndi akazi magareta a m'dziko la Aigupto; nimubwere naye atate wanu.
20. Musasamalire cuma canu; popeza zabwino za dziko lonse la Aigupto ndi zanu.