Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 44:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pamene kudaca, anamukitsa anthu iwo ndi aburu ao.

4. Ataturuka m'mudzi asanamuke patari, Yosefe anati kwa tsanyumba wace, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Cifukwa canji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino?

5. Kodi si ndico comwera naco mbuyanga, naombeza ula naco? Mwacitira coipa pakutero.

6. Ndipo anapeza iwo, nanena nao mau omwewo.

7. Nati kwa iye, Bwanji mbuyanga anena mau otere? Ngati nkutheka kuti akapolo anu acite cotero?

8. Taonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kuturuka m'dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m'nyumba ya mbuyanga kapena siliva kapena golidi?

9. iye wa akapolo anu ampeza naco afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga.

Werengani mutu wathunthu Genesis 44