Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 44:29-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. ndipo ngati mukandicotsera ameneyonso, ndipo ngati cimgwera coipa, mudzanditsitsira ndi cisoni imvi zanga kumanda.

30. Cifukwa cace ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wace uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo;

31. kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi cisoni imvi za atate wathu kumanda.

32. Pakuti kapolo wanu anadziyesa cikole ca mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi cifukwa kwa atate wanga nthawi zonse.

33. Tsopanotu, mtumiki wanu akhale kapolo wa mbuyanga m'malo mwa mnyamata; mnyamatayo akwere pamodzi ndi abale ace.

34. Pakuti ndidzakwera bwanji kwa atate wanga, mnyamatayo akapanda kukhala ndi ine? ndingaone coipa cidzagwera atate wanga.

Werengani mutu wathunthu Genesis 44