10. Ndipo iye mati, Tsononso cikhale monga mwa nau anu: iye amene ampeza naco adzakhala kapolo wanga; ndipo inu nudzakhala opanda cifukwa.
11. Ndipo anafulumira natsitsa pansi zense thumba lace, namasula yense humba lace.
12. Ndipo iye anafunauna kuyambira pa wamkuru naleka pa wamng'ono; nacipeza cikho n'thumba la Benjamini:
13. ndipo anang'amba zobvala zao, nasenzetsa yense buru wace, nabwera kumuzi.