Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 41:32-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo lotolo linabwezedwa kawiri kwa Farao, cifukwa cinthu ciri cokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kucicita.

33. Tsopano, Farao afunefune'munthu wakuzindikira ndi wanzeru, amkhazike iye ayang'anire dziko la Aigupto.

34. Farao acite cotere, alembe woyang'anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Aigupto m'zaka zisanu ndi ziwiri zakucuruka dzinthu.

35. Iwo asonkhanitse cakudya conse ca zaka zabwino izo zirinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale cakudya m'midzi, namsunge.

36. Ndipocakudyacocidzakhalam'dziko cosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Aigupto; kuti dziko lisanonongedwe ndi njala.

37. Ndipo cinthuco cinali cabwino m'maso mwa Farao, ndi m'maso mwa anyamata ace.

38. Ndipo Farao anati kwa anyamata ace, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m'mtima mwace?

39. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe.

40. Uziyang'anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wacifumu pokha ine ndidzakuposa iwe.

41. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Taona, ndakhazika iwe wolamulira dziko lonse la Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Genesis 41