Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 40:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali zitapita izi, wopereka cikho wa mfumu ya Aigupto ndi wophika mkate wace anamcimwira mbuye wao mfumu ya Aigupto.

2. Ndipo Farao anakwiyira akuru ace awiriwo wamkuru wa opereka cikho, ndi wamkuru wa ophika mkate.

3. Ndipo anaika iwo asungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, m'kaidi, umo anamangidwa Yosefe.

4. Ndipo kazembe wa alonda anapereka iwo kwa Yosefe, ndipo iye anawatumikira iwo: ndipo anakhala nthawi mosungidwamo.

5. Ndipo analota maloto onse awiri, yense lata lace, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lace, wopereka cikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aigupto, amene anamangidwa m'kaidi.

6. Ndipo Yosefe analowa kwa iwo m'mawa, nawaona iwo, taonani, anali oziya.

7. Ndipo anafunsa akuru a Farao osungidwa naye m'nyumba ya mbuyace, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero?

Werengani mutu wathunthu Genesis 40