Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 38:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ace nalowa kwa M-adulami, dzina lace Hira.

2. Ndipo Yuda anaona kumeneko mwana wamkazi wa Mkanani dzina lace Sua: ndipo anamtenga, nalowa kwa iye.

3. Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Eri.

4. Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Onani.

5. Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namucha dzina lace Sela: ndipo iye anali pa Kezibi pamene mkazi anambala iye,

6. Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wace woyamba mkazi, ndipo dzina lace ndilo Tamara.

7. Koma Eri mwana wace woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova: ndipo Yehova anamupha iye.

8. Ndipo Yuda anati kwa Onani, Lowani naye mkazi wa mbale wako, ndi kumcitira mkazi zoyenera mphwace wa mwamuna wace, ndi kumuukitsira mkuru wako mbeu.

Werengani mutu wathunthu Genesis 38