Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 37:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yakobo anakhala m'dziko limene anakhalamo mlendo atate wace, m'dziko la Kanani.

2. Mibadwo ya Yakobo ndi iyi: Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ace; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana amuna a Zilipa, akazi a atate wace; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wace mbiri yao yoipa.

3. Koma Israyeli anamkonda Yosefe koposa ana ace onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wace; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro.

4. Ndipo abale ace anaona kuti atate wace anamkonda iye koposa abale ace onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.

5. Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ace; ndipo anamuda iye koposa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 37