Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 36:30-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. mfumu Disoni, mfumu Ezeri, mfumu Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, monga mwa maufumu ao m'dziko la Seiri.

31. Amenewo ndi mafumu analamulira m'dziko la Edomu, asadalamulire ana a Israyeli mfumu ali yense.

32. Ndipo Bela mwana wamwamuna wa Beori, analamulira m'Edomu, ndipo dzina la mudzi wace ndilo Dinaba.

33. Ndipo Bela anamwalira, ndipo Jobabi mwana wamwamuna wa Zera wa ku Bozara analamulira m'malomwace.

34. Ndipo Jobabi anamwalira, ndipo Husami wa ku dziko la Atemani analamulira m'malo mwaceo

35. Ndipo Husami anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midyani m'dambo la Moabu, analamulira m'malo mwace: dzina la mudzi wace ndi Avita.

36. Ndipo Hadadi anamwalira, ndipo Samila wa ku Masereka analamulira m'malo mwace.

37. Ndipo Samila anamwalira, ndipo Sauli wa ku Rehoboti pambali pa Nyanja analamulira m'malo mwaceo

38. Ndipo Sauli anamwalira, ndipo Baal-hanani mwana wamwamuna wa Akibori analamulira m'malo mwace.

39. Ndipo Baal-hanani mwana wamwamuna wa Akibori anamwalira, ndipo Hadari analamulira m'malo mwace; dzina la mudzi wace ndi Pau; ndipo dzina la mkazi wace ndi Mehetabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-zahabi.

40. Maina a mafumu obadwa kwa Esau, monga mabanja ao, monga malo ao, monga maina ao ndi awa: mfumu Timna, mfumu Aliva, mfumu Jeteti:

41. mfumu Oholibama, mfumu Ela, mfumu Pinoni;

42. mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mibezari;

Werengani mutu wathunthu Genesis 36