Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 36:25-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana.

26. Ana a Disoni ndi awa: Hemadani ndi Esibani ndi Itirani, ndi Kerana.

27. Ana a Ezeri ndi awa: Biliha, ndi Zavani, ndi Akani.

28. Ana a Disoni ndi awa: Uzi ndi Arana.

29. Mafumu obadwa kwa Ahori: mfumu Lotani, mfumu Sobali, mfumu Zibeoni, mfumu Ana,

30. mfumu Disoni, mfumu Ezeri, mfumu Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, monga mwa maufumu ao m'dziko la Seiri.

31. Amenewo ndi mafumu analamulira m'dziko la Edomu, asadalamulire ana a Israyeli mfumu ali yense.

32. Ndipo Bela mwana wamwamuna wa Beori, analamulira m'Edomu, ndipo dzina la mudzi wace ndilo Dinaba.

33. Ndipo Bela anamwalira, ndipo Jobabi mwana wamwamuna wa Zera wa ku Bozara analamulira m'malomwace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 36