Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 36:24-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ana a Zibeoni ndi amenewa: Aia ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'cipululu, pakudyetsa aburu a Zibeoni atate wace.

25. Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana.

26. Ana a Disoni ndi awa: Hemadani ndi Esibani ndi Itirani, ndi Kerana.

27. Ana a Ezeri ndi awa: Biliha, ndi Zavani, ndi Akani.

28. Ana a Disoni ndi awa: Uzi ndi Arana.

29. Mafumu obadwa kwa Ahori: mfumu Lotani, mfumu Sobali, mfumu Zibeoni, mfumu Ana,

30. mfumu Disoni, mfumu Ezeri, mfumu Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, monga mwa maufumu ao m'dziko la Seiri.

31. Amenewo ndi mafumu analamulira m'dziko la Edomu, asadalamulire ana a Israyeli mfumu ali yense.

32. Ndipo Bela mwana wamwamuna wa Beori, analamulira m'Edomu, ndipo dzina la mudzi wace ndilo Dinaba.

33. Ndipo Bela anamwalira, ndipo Jobabi mwana wamwamuna wa Zera wa ku Bozara analamulira m'malomwace.

34. Ndipo Jobabi anamwalira, ndipo Husami wa ku dziko la Atemani analamulira m'malo mwaceo

35. Ndipo Husami anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midyani m'dambo la Moabu, analamulira m'malo mwace: dzina la mudzi wace ndi Avita.

36. Ndipo Hadadi anamwalira, ndipo Samila wa ku Masereka analamulira m'malo mwace.

37. Ndipo Samila anamwalira, ndipo Sauli wa ku Rehoboti pambali pa Nyanja analamulira m'malo mwaceo

Werengani mutu wathunthu Genesis 36