Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 36:19-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Amenewa ndi ana amuna a Esau, amenewa ndi mafumu ao; yemweyo ndi Edomu.

20. Amenewa ndi ana amuna a Seiri Mhori, okhala m'dzikomo: Lotani ndi Sobala, ndi Zibeoni, ndi Ana,

21. ndi Disoni ndi Ezeri ndi Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, ana a Seiri, m'dziko la Edomu.

22. Ndi ana a Lotani anali Hori ndi Hemamu: mlongo wace wa Lotani anali Timna.

23. Ana a Sobali ndi awa: Alivani ndi Manahati ndi Ebali, Sefo ndi Onamu.

24. Ana a Zibeoni ndi amenewa: Aia ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'cipululu, pakudyetsa aburu a Zibeoni atate wace.

25. Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana.

Werengani mutu wathunthu Genesis 36