Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 35:17-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo panali pamene anabvutidwa, namwino anati kwa iye, Usaope: pakuti udzakhala ndi mwana wina wamwamuna.

18. Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamucha dzina lace Benoni; koma atate wace anamucha Benjamini.

19. Ndipo anafa Rakele, naikidwa pa njira va ku Efrati (ndipo Betelehemu),

20. Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamanda pace: umenewo ndi coimiritsa ca pa manda a Rakele kufikira lero.

21. Ndipo Israyeli anapita namanga hema wace patseri pa nsanja ya Edere.

22. Ndipo panali pamene Israyeli anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wace: ndipo Israyeli anamva.Ana amuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:

23. ana amuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;

24. ana amuna a Rakele: ndiwo Yosefe ndi Benjamini;

25. ana amuna a Biliha mdzakazi wace wa Rakele: ndiwo Dani ndi Nafitali;

26. ndipo ana amuna a Zilipa mdzakazi wace wa Leya: ndiwo Gadi ndi Aseri: amenewo ndi ana amuna a Yakobo amene anabala iye m'Padanaramu.

27. Ndipo Yakobo anafika kwa Isake atate wace ku Mamre, ku KiriyatiAriba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isake.

28. Ndipo masiku a Isake anali zaka zana limodzi kudza makumi asanu ndi atatu.

29. Ndipo Isake anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wace, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ace amuna anamuika iye.

Werengani mutu wathunthu Genesis 35