13. Ndipo Mulungu anakwera kumcokera iye kumene ananena naye.
14. Ndipo Yakoboanaimiritsamwala pamalo pamene ananena ndi iye, coimiritsa camwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta.
15. Ndipo anacha dzina lace la pamalo pamene Mulungu ananena ndi iye, Beteli.
16. Ndipo anacokera ku Beteli: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efrati: ndipo Rakele anabala nabvutidwa.
17. Ndipo panali pamene anabvutidwa, namwino anati kwa iye, Usaope: pakuti udzakhala ndi mwana wina wamwamuna.
18. Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamucha dzina lace Benoni; koma atate wace anamucha Benjamini.
19. Ndipo anafa Rakele, naikidwa pa njira va ku Efrati (ndipo Betelehemu),
20. Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamanda pace: umenewo ndi coimiritsa ca pa manda a Rakele kufikira lero.
21. Ndipo Israyeli anapita namanga hema wace patseri pa nsanja ya Edere.