Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 35:12-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. ndipo dziko limene ndinapatsa kwa Abrahamu ndi kwa Isake ndidzalipatsa kwa iwe ndipo ndidzapatsa mbeu zako za pambuyo pako dzikoli.

13. Ndipo Mulungu anakwera kumcokera iye kumene ananena naye.

14. Ndipo Yakoboanaimiritsamwala pamalo pamene ananena ndi iye, coimiritsa camwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta.

15. Ndipo anacha dzina lace la pamalo pamene Mulungu ananena ndi iye, Beteli.

16. Ndipo anacokera ku Beteli: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efrati: ndipo Rakele anabala nabvutidwa.

17. Ndipo panali pamene anabvutidwa, namwino anati kwa iye, Usaope: pakuti udzakhala ndi mwana wina wamwamuna.

18. Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamucha dzina lace Benoni; koma atate wace anamucha Benjamini.

19. Ndipo anafa Rakele, naikidwa pa njira va ku Efrati (ndipo Betelehemu),

20. Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamanda pace: umenewo ndi coimiritsa ca pa manda a Rakele kufikira lero.

21. Ndipo Israyeli anapita namanga hema wace patseri pa nsanja ya Edere.

22. Ndipo panali pamene Israyeli anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wace: ndipo Israyeli anamva.Ana amuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:

Werengani mutu wathunthu Genesis 35