Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 33:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pace, nampsompsona; ndipo analira iwo.

5. Ndipo anatukula maso ace nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.

6. Ndipo adzakazi anayandikira ndi ana ao, nawerama pansi.

7. Ndiponso Leya ndi ana ace anayandikira nawerama pansi: pambuyo pace anayandikira Yosefe ndi Rakele, nawerama pansi,

8. Ndipo anati, Nanga khamu lonse limene ndinakomana nalo nlotani? Ndipo anati, Kuti ndipeze ufulu pamaso pa mbuyanga.

9. Ndipo Esau anati, Zanga zindifikira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha.

Werengani mutu wathunthu Genesis 33