Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 32:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. ndipo ndiri nazo ng'ombe ndi aburu, ndi zoweta ndi akapolo ndi adzakazi, ndipo ndatumiza kukuuza mbuyanga kuti ndipeze ufulu pamaso pako.

6. Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.

7. Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, nabvutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamila, zikhale makamu awiri;

8. ndipo anati, Akafika Esau pa khamu limodzi nalikantha, linalo lotsala lidzapulumuka.

9. Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isake, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakucitira iwe bwino:

10. sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamcitira kapolo wanu: cifukwa ndi ndodo yanga ndinaoloka pa Yordano uyu; ndipo tsopano ndiri makamu awiri.

Werengani mutu wathunthu Genesis 32