Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 32:22-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ace awiri, ndi adzakazi ace awiri, ndi ana ace amuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa doko la Yaboki.

23. Ndipo anawatenga iwo nawaolotsa pamtsinje, naziolotsa zonseanalinazo.

24. Ndipo anatsala Yakobo yekha; ndipo analimbana naye munthu kufikira mbandakuca.

25. Ndipo pamene anaona kuti sanamlaka, anakhudza nsukunyu ya ncafu yace; ndipo nsukunyu ya ncafu yace ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye.

26. Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, cifukwa kulinkuca. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.

27. Ndipo iye anati kwa Yakobo, Dzina lako ndani? Nati iye, Yakobo.

28. Ndipo anati, Dzina lako silidzachedwanso Yakobo, koma Israyeli, cifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.

Werengani mutu wathunthu Genesis 32