Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 32:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yakobo anankabe ulendo wace, ndipo amithenga a Mulungu anakomana naye.

2. Pamene Yakobo anawaona anati, Ili ndi khamu la Mulungu: ndipo anacha pamenepo dzina lace Mahanaimu.

3. Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pace kwa Esau mkuru wace, ku dziko la Seiri, ku dera la ku Edomu.

4. Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene cotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano line:

5. ndipo ndiri nazo ng'ombe ndi aburu, ndi zoweta ndi akapolo ndi adzakazi, ndipo ndatumiza kukuuza mbuyanga kuti ndipeze ufulu pamaso pako.

6. Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.

7. Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, nabvutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamila, zikhale makamu awiri;

8. ndipo anati, Akafika Esau pa khamu limodzi nalikantha, linalo lotsala lidzapulumuka.

Werengani mutu wathunthu Genesis 32