4. Ndipo Yakobo anatumiza naitana Rakele ndi Leya adze kubusa ku zoweta zace,
5. ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekera ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.
6. Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu.
7. Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipilo anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andicitire ine coipa.
8. Akati cotero, Zamathotho-mathotho zidzakhala malipilo ako, zoweta zonse zinabala zamathotho-mathotho; ndipo akati iye cotere, Zamipyololo-mipyololo zidzakhala malipilo ako, ziweto zonse zinabala mipyololo-mipyololo.